Yesaya 51:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mverani Ine, inu amene mutsata cilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani ikuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo.

2. Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumcurukitsa.

Yesaya 51