Yesaya 42:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. kuti utsegule maso akhungu, uturutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, aturuke m'nyumba ya kaidi.

8. Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.

9. Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizichula; zisanabuke ndidzakumvetsani.

10. Yimbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ace kucokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse ziri m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.

11. Cipululu ndi midzi yace ikweze mau ao, midzi imene Kedara akhalamo; okhala m'Sela ayimbe, akuwe kucokera pamwamba pa mapiri.

12. Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ace m'zisumbu.

Yesaya 42