Yesaya 31:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Koma Aaigupto ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lace, wothandiza adzapunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.

4. Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yace, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupitikitsa, ngakhale kudzicepetsa wokha, cifukwa ca phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo ku phiri la Ziyoni, ndi kucitunda kwace komwe.

5. Monga mbalame ziuluka, motero Yehova wamakamu adzacinjiriza Yerusalemu; Iye adzacinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga.

6. Bwerani kwa Iye amene mwampandukira kolimba, ana a Israyeli inu.

7. Pakuti tsiku limenelo iwo adzataya munthu yense mafano ace asiliva, ndi mafano ace agolidi amene manja anu anu anawapanga akucimwitseni inu.

8. Pamenepo Asuri adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammariza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ace adzalamba.

9. Ndipo mwala wace udzacoka, cifukwa ca mantha, ndi akalonga ace adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wace uli m'Ziyoni, ndi ng'anjo yace m'Yerusalemu.

Yesaya 31