5. Iwo onse adzakhala ndi manyazi, ndi anthu amene sangapindule nao kanthu, amene sakhala kwa iwo thangata, pena phindu, koma manyazi ndi citonzo.
6. Katundu wa zirombo za kumwera.M'dziko lobvuta ndi lopweteka, kumeneko kucokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula cuma cao pamsana pa aburu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamila, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.
7. Pakuti thangata la Aigupto liri lacabe, lopanda pace; cifukwa cace ndamucha wonyada, wokhala cabe.
8. Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe ku nthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse.