Yesaya 3:23-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. akalirole, ndi nsaru zabafuta, ndi nduwira, ndi zophimba.

24. Ndipo padzakhala m'malo mwa zotsekemera mudzakhala zobvunda; ndi m'malo mwa lamba cingwe; ndipo m'malo mwa tsitsi labwino dazi; m'malo mwa cobvala ca pacifuwa mpango waciguduli; zipsera m'malo mwa ukoma.

25. Amuna ako adzagwa ndi lupanga, ndi wamphamvu wako m'nkhondo.

26. Ndipo zipata zace zidzalira maiko; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.

Yesaya 3