13. Yehova aimirira kuti atsutsane, naimiriranso kuti aweruze mitundu ya anthu.
14. Yehova adzalowa monenera mirandu ndi okalamba a anthu ace, ndi akuru ace: Ndinu amene mwadya munda wamphesa, zofunkha za waumphawi ziri m'nyumba zanu;
15. muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? ati Ambuye Yehova wa makamu.
16. Komanso Yehova ati, Cifukwa kuti ana akazi a Ziyoni angodzikuza atakweza makosi ao, ndi maso ao adama nayenda nanyang'ama poyenda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao;
17. cifukwa cace Ambuye adzacita nkanambo pa liwombo la ana akazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzabvundukula m'cuuno mwao.
18. Tsiku limenelo Ambuye adzacotsa zigwinjiri zao zokoma, ndi zitunga, ndi mphande;
19. mbera, ndi makoza, ndi nsaru za pankhope;