7. Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi cakumwa caukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, adzandima popenya, napunthwa poweruza.
8. Pakuti magome onse adzazidwa ndi masanzi ndi udio, palibe malo okonzeka.
9. Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? iwo amene aletsedwa kuyamwa, nacotsedwa pamabere?
10. Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono.
11. Iai, koma ndi anthu a milomo yacilendo, ndi a lilume lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa;
12. amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva.
13. Cifukwa cace mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa cambuyo, ndi kutyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.