9. Komanso iwo amene agwira nchito yakupala bwazi, ndi iwo amene aomba nsaru yoyera, adzakhala ndi manyazi.
10. Ndipo maziko ace adzasweka, onse amene agwira nchito yolipidwa adzabvutidwa mtima.
11. Akalonga a Zoani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru a Farao wasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale?
12. Nanga tsopano anzeru ali kuti? akuuze iwe tsopano; adziwe cimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kucitira Aigupto.
13. Akalonga a Zoani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asoceretsa Aigupto, amene ali mwala wa pangondya wa mapfuko ace.
14. Yehova wasanganiza mzimu wa kusaweruzika pakati pace; ndipo iwo asoceretsa Aigupto m'nchito zonse zace, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pace.
15. Aigupto sadzakhala ndi nchito, imene mutu pena mcira, pena nthambi ya kanjedza, pena mlulu zidzaigwira.