Yesaya 19:20-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo cidzakhala cizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Aigupto; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, cifukwa ca osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.

21. Ndipo Yehova adzadziwika kwa Aigupto, ndipo Aaigupto adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kucitadi.

22. Ndipo Yehova adzakantha Aigupto kukantha ndi kuciritsa; ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova, ndipo Iye adzapembedzedwa ndi iwo, nadzawaciritsa.

23. Tsiku limenelo padzakhala khwalala locokera m'Aigupto kunka ku Asuri, ndipo M-asuri adzafika ku Aigupto, ndi M-aigupto adzafika ku Asuri, ndipo Aaigupto adzapembedzera pamodzi ndi Aasuri.

24. Tsiku limenelo Israyeli ndi Aigupto ndi Asuri atatuwa, adzakhala mdalitso pakati pa dziko lapansi;

Yesaya 19