19. Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati pa dziko la Aigupto, ndi coimiritsa ca Yehova m'malire ace.
20. Ndipo cidzakhala cizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Aigupto; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, cifukwa ca osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.
21. Ndipo Yehova adzadziwika kwa Aigupto, ndipo Aaigupto adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kucitadi.