Yesaya 18:5-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakuti masika asanafike, kutatha kuphuka ndi posanduka duwa mphesa yofuna kucha, iye adzadzombolera tinthambi ndi mphopo, ndi nthambi zotasa adzazicotsa ndi kuzisadza.

6. Adzasiyira mbalame zakulusa za m'mapiri ndi zirombo za dziko nthambizo, ndipo mbalame zakulusa zidzakhalapo m'dzinja, ndi zirombo zonse za dziko zidzakhalapo m'malimwe.

7. Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu atari ndi osalala, yocokera kwa mtundu woopsya cikhalire cao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lace nyanja ziligawa, ku malo a dzina la Yehova wa makamu, phiri la Ziyoni.

Yesaya 18