1. Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wacoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.
2. Taonani, Mulungu ndiye cipulumutso canga; ndidzakhulupira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye cipulumutso canga.
3. Cifukwa cace mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za cipulumutso.