17. Ndipo kuwala kwa Israyeli kudzakhala moto, ndi Woyera wace adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yace ndi lunguzi wace tsiku limodzi.
18. Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m'nkhalango yace, ndi wa m'munda wace wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera.
19. Ndipo mitengo yotsala ya m'nkhalango yace idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera.
20. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israyeli, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israyeli, ntheradi.
21. Otsala adzabwera, otsala a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu.