Yeremiya 9:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Mucenjere naye yense mnansi wace, musakhulupirire yense mbale wace; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.

5. Ndipo yense adzanyenga mnansi wace, osanena coonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kucita zoipa.

6. Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.

7. Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzacitanji, cifukwa ca mwana wamkazi wa anthu anga?

8. Lilime lao ndi mubvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wace pakamwa pace, koma m'mtima mwace amlalira.

9. Kodi sindidzawalanga cifukwa ca izi? ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera cilango mtundu wotere?

10. Cifukwa ca mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, cifukwa ca mabusa a cipululu ndidzacita maliro, cifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.

Yeremiya 9