Yeremiya 50:35-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Lupanga liri pa Akasidi, ati Yehova, pa okhala m'Babulo, pa akuru ace, ndi pa anzeru ace.

36. Lupanga liri pa amatukutuku, ndipo adzapusa; lupanga liri pa anthu olimba ace, ndipo adzaopa.

37. Lupanga liri pa akavalo ao, ndi pa magareta ao, ndi pa anthu onse osanganizidwa amene ali pakati pace, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga liri pa cuma cace, ndipo cidzalandidwa.

Yeremiya 50