10. Kwerani pa makoma ace nimupasule; koma musatsirize konse; cotsani nthambi zace pakuti siziri za Yehova.
11. Pakuti nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda zinandicitira monyenga kwambiri, ati Yehova.
12. Akana Yehova, ndi kuti, Si ndiye; coipa sicidzatifika ife; sitidzaona kapena lupanga kapena njala;
13. ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; comweco cidzacitidwa ndi iwo.
14. Cifukwa cace Yehova Mulungu wa makamu atero, Cifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.