Yeremiya 49:32-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo ngamila zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng'ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira ku mphepo zonse iwo amene ameta m'mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao ku mbali zao zonse, ati Yehova.

33. Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lacikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.

34. Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiya mneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti,

35. Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao.

36. Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai ku mbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo ku mphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opitikitsidwa a Elamu sadzafikako.

37. Ndipo ndidzacititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera coipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha;

38. ndipo ndidzaika mpando wacifumu wanga m'Elamu, ndipo ndidzaononga pamenepo mfumu ndi akulu, ati Yehova.

39. Koma padzaoneka masiku akutsiriza, kuti ndidzabwezanso undende wa Elamu, ati Yehova.

Yeremiya 49