17. Inu nonse akumzungulira, mumcitire iye cisoni, inu nonse akudziwa dzina lace; muti, Cibonga colimba catyokatu, ndodo yokoma!
18. Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Moabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.
19. Iwe wokhala m'Aroeri, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Cacitidwa ciani?
20. Moabu wacitidwa manyazi, pakuti watyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Moabu wapasuka.