5. Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'cidikha cao; udzadziceka masiku angati?
6. Iwe lupanga la Yehova, atsala masiku angati osakhala cete iwe? dzilonge wekha m'banzi lako; puma, nukhale cete.
7. Udzakhala cete bwanji, popeza Yehova anakulangiza? za Asikeloni, ndi za m'mbali mwa nyanja, pamenepo analiika.