14. Nenani m'Aigupto, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.
15. Akulimba ako akokoledwa bwanji? sanaime, cifukwa Yehova anawathamangitsa,
16. Anapunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzace, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, ku dziko la kubadwa kwathu, kucokera ku lupanga lobvutitsa.
17. Ndipo anapfuula kumeneko, Farao mfumu ya Aigupto ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira,