26. Cifukwa cace tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m'dziko la Aigupto: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikuru, ati Yehova, kuti dzina langa silidzachulidwanso m'kamwa mwa munthu ali yense wa Yuda m'dziko la Aigupto, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu.
27. Taonani, ndiwayang'anira kuwacitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Aigupto adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.
28. Ndipo iwo amene adzapulumuka kulupanga adzabwera kuturuka ku dziko la Aigupto kulowa m'dziko la Yuda, owerengeka; ndipo otsala onse a Yuda, amene analowa m'dziko la Aigupto kuti akhale m'menemo, adzadziwa ngati adzatsimikizidwa mau a yani, kapena anga, kapena ao.
29. Ndipo ici cidzakhala cizindikiro ca kwa inu, ati Yehova, cakuti Ine ndidzakulangani m'malo muno, kuti mudziwe kuti mau anga adzatsimikizidwatu akucitireni inu zoipa.
30. Yehova atero: Taonani, ndidzapereka Farao Hofra mfumu ya Aigupto m'manja a adani ace, ndi m'manja a iwo akufuna moyo wace; monga ndinapereka Zedekiya mfumu ya Yuda m'manja a Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo mdani wace, amene anafuna moyo wace.