4. Ndipo Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvera mau a Yehova, kuti akhale m'dziko la Yuda.
5. Koma Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse: a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera ku mitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda;
6. ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao Wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wace wa Ahikamu, mwana wace wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wace wa Neriya;
7. ndipo anadza nalowa m'dziko la Aigupto; pakuti sanamvera mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.
8. Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yeremiya m'Tapanesi, kuti,