8. pamenepo anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, ndi Saraya mwana wa Tanumeti, ndi ana a Efai wa ku Netofa, ndi Jezaniya mwana wa munthu wa ku Maaka, iwo ndi anthu ao.
9. Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Akasidi; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babulo, ndipo kudzakukomerani.
10. Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Akasidi, amene adzadza kwa ife; koma inu, sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'midzi imene mwailanda.
11. Comweco pamene Ayuda onse okhala m'Moabu ndi mwa ana a Amoni, ndi m'Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babulo inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;
12. pamenepo Ayuda onse anabwerera kufumira ku malo onse kumene anawaingitsirako, nafika ku dziko la Yuda, kwa Gedaliya, ku Mizipa, nasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamalimwe zambiri.
13. Ndiponso Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala m'minda, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa,