Yeremiya 4:24-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka.

25. Ndinaona, ndipo taona, panalibe munthu, ndi mbalame zonse zakumwamba zinathawa.

26. Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali cipululu, ndipo midzi yace yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wace woopsya.

Yeremiya 4