3. Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukali mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maseya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.
4. Ndipo Yeremiya analikuyendayenda mwa anthu; cifukwa asanamuike iye m'nyumba yandende.
5. Ndipo nkhondo ya Farao inaturuka m'Aigupto; ndipo pamene Akasidi omangira misasa Yerusalemu anamva mbiri yao, anacoka ku Yerusalemu.
6. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya mneneri, kuti,
7. Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakuturukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Aigupto ku dziko lao.