Yeremiya 32:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

7. Taonani, Hanameli mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.

8. Ndipo Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.

9. Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanameli mwana wa cibale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekele khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.

10. Ndipo ndinalemba cikalataco, ndicisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m'miyeso.

11. Ndipo ndinatenga kalata wogulira, wina wosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi wina wobvundukuka;

Yeremiya 32