Yeremiya 32:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova caka cakhumi ca Zedekiya mfumu ya Yuda, cimene cinali caka cakhumi ndi cisanu ndi citatu ca Nebukadirezara.

2. Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babulo inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali ku nyumba ya mfumu ya Yuda.

Yeremiya 32