6. Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; cifukwa canji ndiona mwamuna ndi manja ace pa cuuno cace, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?
7. Kalanga ine! pakuti nlalikuru tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.
8. Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzatyola gori lace pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;