Yeremiya 3:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Kodi kuyambira tsopano sudzapfuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu?

5. Kodi adzasunga mkwiyo wace ku nthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka cimariziro? Taona, wanena ndi kucita zoipa monga unatero.

6. Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona cimene wacicita Israyeli, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri atari onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kucita dama pamenepo.

7. Ndipo ndinati atacita zimenezo zonse, Adzabwera kwa Ine; koma sanabwere, ndipo mphwace wonyenga, Yuda, anaona.

8. Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamcotsa Israyeli wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata wacilekaniro cifukwa ca kucita cigololo iye, mphwace Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nacita dama.

9. Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lace inaipitsa dziko, ndipo anacita cigololo ndi miyala ndi mitengo.

10. Ndipo zingakhale zonsezi mphwace wonyenga sanabwera kwa Ine ndi mtima wace wonse, koma monama, ati Yehova.

11. Ndipo Yehova anati kwa ine, Israyeli wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga,

Yeremiya 3