Yeremiya 3:2-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Kwezera maso ako ku mapiri oti se, nuone: sanagona ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga M-arabu m'cipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.

3. Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.

4. Kodi kuyambira tsopano sudzapfuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu?

5. Kodi adzasunga mkwiyo wace ku nthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka cimariziro? Taona, wanena ndi kucita zoipa monga unatero.

Yeremiya 3