14. Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzi mmodzi wa pa mudzi uli wonse, ndi awiri awiri a pa banja liri lonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni;
15. ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.
16. Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kucuruka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la cipangano ca Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzacitanso konse.
17. Pa nthawi yomweyo adzacha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa.