Yeremiya 28:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzacitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.

10. Pamenepo Hananiya anacotsa gori pa khosi la Yeremiya, nalityola.

11. Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Comweco ndidzatyola gori la Nebukadinezara mfumu ya Babulo zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulicotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anacoka.

12. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, atatyola Hananiya mneneri gori kulicotsa pa khosi la Yeremiya, kuti,

13. Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Watyola magori amtengo; koma udzapanga m'malo mwao magori acitsulo.

14. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ndaika gori lacitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama za kuthengo.

Yeremiya 28