Yeremiya 25:32-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzaturuka ku mtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kucokera ku malekezero a dziko lapansi.

33. Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kucokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dzikolapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.

34. Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akuru a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati cotengera cofunika.

35. Ndipo abusa adzasowa pothawira, mkuru wa zoweta adzasowa populumukira.

Yeremiya 25