Yeremiya 22:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova atero: Tsikira ku nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi kunena komweko mau awa,

2. ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.

Yeremiya 22