Yeremiya 20:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma, Inu Yehova wa makamu, amene muyesa olungama, amene muona imso ndi mtima, mundionetse ine kubwezera cilango kwanu pa iwo; pakuti kwa inu ndaululira mlandu wanga.

13. Muyimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m'dzanja la ocita zoipa.

14. Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa; lisadalitsike tsiku limene amai wanga anandibala ine.

15. Atembereredwe munthu amene anatengera mau kwa atate wanga, kuti, Mwana wamwamuna anakubadwira iwe; ndi kumsekeretsatu iye.

16. Munthuyo akhale ngati midzi imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mpfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;

17. cifukwa sanandipha ine m'mimba; kuti mai wanga akhale manda anga, ndi mimba yace yaikuru nthawi zonse.

18. Cifukwa canji ndinaturuka m'mimba kuti ndione kutopa ndi kulira, kuti masiku anga athe ndi manyazi?

Yeremiya 20