Yeremiya 19:10-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pamenepo uziphwanya nsupa pamaso pa anthu otsagana ndi iwe,

11. nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Comweco ndidzaphwanya anthu awa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kulumbanso, ndipo adzaika maliro m'Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo.

12. Ndidzatero ndi malo ano, ati Yehova, ndi okhalamo, kusanduliza mudzi uwu ngati Tofeti;

Yeremiya 19