Yeremiya 18:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. koma ukacita coipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka cabwinoco, ndidati ndiwacitire.

11. Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu coipa, ndilingalira inu kanthu kakucitira inu coipa; mubwerere tsono inu nonse, yense ku njira yace yoipa, nimukonze njira zanu ndi macitidwe anu.

12. Koma iwo ati, Palibe ciyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzacita yense monga mwa kuuma kwa mtima wacewoipa.

13. Cifukwa cace atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israyeli wacita cinthu coopsetsa kwambiri.

14. Kodi matalala a Lebano adzalephera pa mwala wa m'munda? kodi adzaphwa madzi ozizira otsika kutari?

Yeremiya 18