14. Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako ku dziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m'mkwiyo wanga, umene udzatentha inu.
15. Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire ine, mundibwezere cilango pa ondisautsa ine; musandicotse m'cipiriro canu; dziwani kuti cifukwa ca Inu ndanyozedwa.
16. Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine cikondwero ndi cisangalalo ca mtima wanga; pakuti ndachedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.
17. Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekera-sekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha cifukwa ca dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.
18. Kupweteka kwanga kuti cipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?