Yeremiya 13:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Tamvani inu, Cherani khutu; musanyade, pakuti Yehova wanena.

16. Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanakhumudwe pa mapiri acizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Ive asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.

17. Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri cifukwa ca kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, cifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.

18. Nenani kwa mfumu ndi kwa amace wa mfumu, Dzicepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.

19. Midzi ya ku Mwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda wonse wacotsedwa m'ndende wonsewo, wacotsedwa m'nsinga.

Yeremiya 13