1. Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'cuuno mwako, usauike m'madzi.
2. Ndipo ndinagula mpango monga mwa mau a Yehova, ndi kubvala m'cuuno mwanga.
3. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yaciwiri, kuti,
4. Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'cuuno mwako, nuuke, nupite ku Firate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala.