Yeremiya 11:6-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau onsewa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwacita.

7. Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawaturutsa iwo ku dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga.

8. Koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; cifukwa cace ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti acite, koma sanacita.

Yeremiya 11