1. Zicokera kuti nkhondo, zicokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizicokera ku zikhumbitso zanu zocita nkhondo m'ziwalo zanu?
2. Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimucita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimucita nkhondo; mulibe kanthu, cifukwa simupempha.
3. Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukacimwaze pocita zikhumbitso zanu.