22. Khalani akucita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.
23. Pakuti ngati munthu ali wakumva mau wosati wakucita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yace ya cibadwidwe cace m'kalirole;
24. pakuti wadziyang'anira yekha nacoka, naiwala pompaja nali wotani.
25. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero cipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakucita nchito, adzakhala wodala m'kucita kwace.