Tito 3:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka,

5. zosati zocokera m'nchito za m'cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,

6. amene anatsanulira pa ife mocurukira, mwa Yesu Kristu Mpulumutsi wathu;

7. kuti poyesedwa olungama ndi cisomo ca Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa ciyembekezo ca moyo wosatha.

8. Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a nchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;

Tito 3