Tito 3:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa nchito iri yonse yabwino;

2. asacitire mwano munthu ali yense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere cifatso conse pa anthu onse.

3. Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akucitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundu mitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzace.

4. Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka,

Tito 3