4. kuti akalangize akazi ang one akonde amuna ao, akonde ana ao,
5. akhale odziletsa, odekha, ocita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angacitidwe mwano.
6. Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa;
7. m'zonse udzionetsere wekha citsanzo ca nchito zabwino; m'ciphunzitse cako uonetsere cosabvunda, ulemekezeko,
8. mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana acite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.
9. Akapolo amvere ambuye ao a iwo okha, nawakondweretse m'zonse; osakana mau ao;
10. osatapa pa zao, komatu aonetsere cikhulupiriko conse cabwino; kuti akakometsere ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse.