Rute 4:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. ndipo ndati ndikuululira ici, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso pa akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola.

5. Nati Boazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmoabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa colowa cace.

6. Ndipo woombolerayo anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge colowa canga; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.

7. Koma kale m'Israyeli pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu abvula nsapato yace, naipereka kwa mnansi wace; ndiwo matsimikizidwe m'Israyeli.

Rute 4