7. Naturuka iye kumene anakhalako ndi apongozi ace awiri pamodzi naye; namka ulendo wao kubwererakudzikola Yuda.
8. Ndipo Naomi anati kwa apongozi ace awiri, Mukani, bwererani yense wa inu ku nyumba ya amai wace; Yehova akucitireni zokoma, monga umo munacitira akufa aja ndi ine.
9. Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wace. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi.
10. Ndipo ananena naye, Iai, koma tidzapita nanu kwa anthu a kwanu.
11. Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? ngati ndiri nao m'mimba mwanga ana amuna ena kuti akhale amuna anu?
12. Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindikhoza kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndiri naco ciyembekezo, ndikakhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana amuna;
13. kodi mudzawalindirira akakula? mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti candiwawa koposa cifukwa ca inu popeza dzanja la Yehova landiturukira.
14. Nakweza iwo mau ao, naliranso misozi; ndi Olipa anampsompsona mpongozi wace, koma Rute anamkangamira.
15. Pamenepo anati, Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwao, ndi kwa mulungu wace, bwerera umtsate mbale wako.