43. Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m'minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkuturuka m'mudzi; nawaukira iye nawakantha.
44. Ndi Abimeleki ndi magulu okhala naye anathamanga naima polowera pa cipata ca mudzi; ndi magulu awiriwo anagwera onse okhala m'munda, nawakantha.
45. Ndipo Abimeleki analimbana ndi mudzi tsiku lija lonse; nalanda mudzi nawapha anthu anali m'mwemo; napasula mudzi; nawazapo mcere.
46. Ndipo pamene eni ace onse a nsanja ya ku Sekemu anacimva, analowa m'ngaka ya nyumba ya Eliberiti.
47. Ndipo anauza Abimeleki kuti amuna onse a nsanja ya ku Sekemu asonkhane.