4. Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pace ndi opepuka amene anamtsata.
5. Ndipo anamuka ku nyumba ya atate wace ku Ofira, nawapha abale ace ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.
6. Pamenepo anasonkhana eni ace onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa coimiritsa ciri m'Sekemu.
7. Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu pa phiri la Gerizimu, nakweza mau ace, napfuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ace a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.
8. Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo waazitona, Ukhale iwe mfumu yathu.
9. Koma mtengo waazitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?